Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 30:3 - Buku Lopatulika

Ndipo mkazi akachitira Yehova chowinda, nakadzimanga nacho chodziletsa, pokhala ali m'nyumba ya atate wake, mu unamwali;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mkazi akachitira Yehova chowinda, nakadzimanga nacho chodziletsa, pokhala ali m'nyumba ya atate wake, m'unamwali;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mkazi akakhala mtsikana, nakhalabe m'nyumba ya bambo wake, ndipo alumbira kwa Chauta kuti adzachitadi zina zake zimene walumbira,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Pamene munthu wamkazi amene akukhalabe mʼnyumba ya abambo ake alumbira kwa Yehova kuti adzachita zimene walonjeza pa ubwana wake,

Onani mutuwo



Numeri 30:3
10 Mawu Ofanana  

Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.


Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene munthu achita chowinda cha padera, anthuwo azikhala a Yehova monga mwa kuyesa kwako.


Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake.


ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga nacho moyo wake, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;


Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.


Ndipo ana a Israele sanawakanthe, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga.


Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.


nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.