Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 14:34 - Buku Lopatulika

34 Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Akazi akhale chete m'Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 akazi akhale chete m'misonkhano ya mpingo, pakuti iwo saloledwa kulankhula. Monga Malamulo a Mose anenera, akazi azikhala omvera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Amayi akhale chete mʼmisonkhano ya mpingo. Iwo asaloledwe kuyankhula, koma azikhala omvera monga mmene lamulo linenera.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 14:34
15 Mawu Ofanana  

Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.


Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?


Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.


Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.


Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.


Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.


Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.


Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.


akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa