Numeri 30:4 - Buku Lopatulika4 ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga nacho moyo wake, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga moyo wake nacho, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 tsono bambo wake nkumva za kulumbira kwakeko ndi za malonjezo amene walumbira kuti adzachitadi, koma bambo wakeyo osalankhula kanthu, mwanayo achitedi zimene adalumbirazo. Ayenera kuchitadi zonse zimene walonjezazo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 abambo ake namva kulumbira kwakeko kapena kulonjeza kwake kuti adzachitadi, ndipo abambo akewo wosayankhula kanthu, mkaziyo achitedi zomwe analumbirazo. Ayenera kudzachita zonse zimene walonjeza zija. Onani mutuwo |