Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.
Numeri 3:51 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mose adapereka ndalama zoombolerazo kwa Aroni ndi kwa ana ake, potsata mau amene Chauta adalamula Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anapereka ndalama zowombolera zija kwa Aaroni ndi ana ake aamuna monga mwa mawu amene Yehova analamulira. |
Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.
Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.
Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.
analandira ndalamazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israele; masekeli chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.
Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.
Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;