Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 3:47 - Buku Lopatulika

ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

utenge masekeli asiliva asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale olingana ndi masekeli asiliva a ku malo opatulika kumene sekeli imodzi ikwanira magera makumi aŵiri.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

utenge masekeli asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale ofanana ndi masekeli a ku malo wopatulika, kumene sekeli imodzi imakwanira magera makumi awiri.

Onani mutuwo



Numeri 3:47
10 Mawu Ofanana  

Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.


Golide yense anachita naye mu ntchito yonse ya malo opatulika, golide wa choperekacho, ndicho matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.


Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo muyeso wa mina wanu.


Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika sekeli ndi magera makumi awiri.


Ukayesa wamwamuna wa zaka makumi awiri kufikira wina wa zaka makumi asanu ndi limodzi, uziwayesera a masekeli makumi asanu a siliva, monga mwa sekeli wa malo opatulika.


Akakhala mwana wa mwezi umodzi kufikira zaka zisanu, uziwayesera wamwamuna wa masekeli asanu a siliva, ndi wamkazi wa masekeli atatu a siliva.


Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za mwezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndalama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.


nupereke ndalama zimene akuposawo anaomboledwa nazo kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna.


analandira ndalamazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israele; masekeli chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;