Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za mwezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndalama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za mwezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndalama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 (Muzimuwombola akakhala wa mwezi umodzi). Uike mtengo wake woombolera kuti ukhale ndalama zisanu zasiliva, molingana ndi ndalama za ku malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:16
9 Mawu Ofanana  

Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.


Golide yense anachita naye mu ntchito yonse ya malo opatulika, golide wa choperekacho, ndicho matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.


Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo muyeso wa mina wanu.


Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika sekeli ndi magera makumi awiri.


Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.


Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake paguwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.


Kunena za mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza atatuwo oyamba kubadwa a ana a Israele, akuposa Alevi, akaomboledwe,


ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa