Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:17 - Buku Lopatulika

17 Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake paguwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake pa guwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma mwanawang'ombe woyamba kubadwa kapena mwanawankhosa woyamba kubadwa, kapenanso mwanawambuzi woyamba kubadwa, musaŵaombole. Amenewo ngoyera. Muwaze magazi ao pa guwa, ndipo mutenthe mafuta ao kuti akhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:17
5 Mawu Ofanana  

Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo paguwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova.


Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za mwezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndalama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa