Numeri 18:15 - Buku Lopatulika15 Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Chinthu chilichonse choyamba kubadwa, kaya ndi munthu kaya nyama, chimene amapereka kwa Chauta, chikhale chanu, Komabe mwana wamwamuna wachisamba muzimuwombola, ndiponso pakati pa nyama zosayenera kuzipereka ku nsembe, mwana wake woyamba kubadwa muzimuwombola. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. Onani mutuwo |
ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.