Ndipo mkulu wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi olindira pakhomo atatu;
Numeri 3:32 - Buku Lopatulika Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pamalo opatulika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pa malo opatulika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Eleazara mwana wa wansembe Aroni, ndiye amene anali mkulu wa atsogoleri a Alevi, ndiponso amene ankayang'anira iwo amene ankasamala malo opatulika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtsogoleri wamkulu wa Alevi anali Eliezara mwana wa Aaroni wansembe. Iye anasankhidwa kukhala woyangʼanira omwe ankasamalira malo wopatulika. |
Ndipo mkulu wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi olindira pakhomo atatu;
mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.
Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa chihema chonse, ndi zonse zili m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zake.
Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.
owerengedwa ao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.
koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.