Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 3:31 - Buku Lopatulika

Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikapo nyali, ndi magome a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo ntchito imene iwo adapatsidwa inali yosamala Bokosi lachipangano, tebulo, choikaponyale, maguwa, zipangizo za m'malo opatulika zimene ansembe ankagwirira ntchito, pamodzi ndi nsalu yochingira. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo ankagwira ntchito yosamalira Bokosi la Chipangano, tebulo, choyikapo nyale, maguwa, zipangizo za kumalo wopatulika zimene ansembe ankagwiritsa ntchito, katani, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito.

Onani mutuwo



Numeri 3:31
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Bezalele anapanga likasa la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu;


Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba.


Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele.


Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pamalo opatulika.


Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.


Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.