Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pamalo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pa malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tsono Eleazara mwana wa wansembe Aroni, ndiye amene anali mkulu wa atsogoleri a Alevi, ndiponso amene ankayang'anira iwo amene ankasamala malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Mtsogoleri wamkulu wa Alevi anali Eliezara mwana wa Aaroni wansembe. Iye anasankhidwa kukhala woyangʼanira omwe ankasamalira malo wopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:32
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mkulu wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi olindira pakhomo atatu;


mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.


Ndipo anati kwa ine, Kanyumba aka koloza kumwera nka ansembe odikira Kachisi.


Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.


Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo Amerari; ndiwo mabanja a Merari.


Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa chihema chonse, ndi zonse zili m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zake.


Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.


owerengedwa ao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.


koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa