Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 pamodzi ndi Elizafani, mwana wa Uziyele, amene anali mutu wa mabanja a Akohati,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Kohati anali Elizafani mwana wa Uzieli.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:30
7 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Uziyele ndiwo: Misaele, ndi Elizafani, ndi Sitiri.


Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono.


Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.


Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumwera.


Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.


Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.


Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa