Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.
Numeri 3:29 - Buku Lopatulika Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumwera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya Kachisi ya kumwera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mabanja a ana a Kohati ankamanga zithando zao kumwera kwa chihema cha Mulungu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mabanja a ana a Kohati ankamanga misasa yawo kummwera kwa Chihema. |
Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.
Mbendera ya chigono cha Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.
Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pamalo opatulika.
Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele.