Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:28 - Buku Lopatulika

28 Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pamalo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pa malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Potsata chiŵerengero cha amuna onse kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo, onse anali 8,600, amene ankagwira ntchito m'malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Chiwerengero cha amuna onse a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 8,600. Akohati ankagwira ntchito yosamalira malo wopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:28
5 Mawu Ofanana  

Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.


Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumwera.


Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.


Ndipo azisunga udikiro wake, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la chihema chokomanako, kuchita ntchito ya Kachisi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa