Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
Numeri 3:12 - Buku Lopatulika Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pakati pa Aisraele, ndaŵapatula Alevi, m'malo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa, amene amatsekula mimba ya mai wake. Aleviwo ndi anga, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pakati pa Aisraeli onse ndatenga Alevi kulowa mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kwa amayi a Chiisraeli. Alevi ndi anga, |
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
Ndipo unditengere Ine Alevi (Ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israele.
Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.
Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.