Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo unditengere Ine Alevi (Ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo unditengere Ine Alevi (Ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Tsono unditengere Alevi m'malo mwa ana achisamba onse pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa pakati pa ng'ombe za Aisraele, Ine ndine Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Unditengere Alevi onse mʼmalo mwa ana oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso ziweto zazimuna za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa za Aisraeli. Ine ndine Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:41
10 Mawu Ofanana  

Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.


Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga.


Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse mu Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.


Ndipo Mose anawawerenga, monga Yehova adamuuza, oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele.


Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.


Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.


monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


amene anadzipereka yekha chiombolo m'malo mwa onse; umboni m'nyengo zake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa