Numeri 27:5 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adapita ndi mlandu umenewu pamaso pa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova |
Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.
Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.
Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu.
nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.
Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.