Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
Numeri 27:3 - Buku Lopatulika Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana amuna. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Bambo wathu adafera m'chipululu. Iyeyo sanali nao m'gulu la anthu aja amene adasonkhana pamodzi ndi Kora naukira Chauta, iye adafera tchimo lake, koma analibe ana aamuna. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna. |
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo.
Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.
Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.
Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana aakazi a Zelofehadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti,
Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu.
Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.
Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.
Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.
kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.