Numeri 14:35 - Buku Lopatulika35 Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201435 Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa35 Ine Chauta ndanena. Ndithudi, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oipaŵa, amene agwirizana kuti andiwukire. M'chipululu mommuno ndimo m'mene athere, ndipo afera mommuno.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero35 Ine Yehova, ndanena, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oyipawa, amene agwirizana kunditsutsa. Adzathera mʼchipululu momwe muno, adzafera muno basi.” Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.