Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 26:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana aakazi a Zelofehadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Koma Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi okhaokha. Ana aakazi a Zelofehadi anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:33
5 Mawu Ofanana  

ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Hefere, ndiye kholo la banja la Ahefere.


Pamenepo anayandikiza ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.


Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.


Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana aamuna koma ana aakazi ndiwo; ndipo maina a ana ake aakazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa