Numeri 26:54 - Buku Lopatulika Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Fuko lalikulu ulipatse choloŵa chachikulu, fuko laling'ono choloŵa chaching'ono. Fuko lililonse lilandire choloŵa chake molingana ndi chiŵerengero cha anthu ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa. |
Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,
Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani.
Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.
Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.
Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?
M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao.