Numeri 35:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Pamene mukupatula mizinda imeneyi pa choloŵa cha Aisraele, muchotse mizinda yambiri pa mafuko aakulu, ndipo muchotse mizinda pang'ono pa mafuko aang'ono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa choloŵa chimene lalandira.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Pamene mukupatula midzi imeneyi pa cholowa cha Aisraeli, muchotsepo midzi yambiri pa mafuko aakulu, ndipo midzi pangʼono pa mafuko aangʼono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa cholowa chimene lalandira.” Onani mutuwo |