Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 26:55 - Buku Lopatulika

55 Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Koma dzikolo uligaŵe mwamaere. Alandire choloŵa chao potsata kuchuluka kwa maina a mafuko a makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:55
21 Mawu Ofanana  

Maere aponyedwa pamfunga; koma ndiye Yehova alongosola zonse.


Maere aletsa makangano, nulekanitsa amphamvu.


Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele.


Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere.


Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.


Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;


nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.


Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.


ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;


Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale cholowa chao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.


Cholowa chao chinachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko la hafu.


Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?


Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ake; ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu.


Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.


Ndipo maere achitatu anakwerera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a cholowa chao anafikira ku Saridi;


Maere achinai anamtulukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao.


Ndipo maere achisanu analitulukira fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao.


Maere achisanu ndi chimodzi anatulukira ana a Nafutali, ana a Nafutali monga mwa mabanja ao.


Maere achisanu ndi chiwiri anatulukira fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa