Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 26:54 - Buku Lopatulika

54 Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

54 Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

54 Fuko lalikulu ulipatse choloŵa chachikulu, fuko laling'ono choloŵa chaching'ono. Fuko lililonse lilandire choloŵa chake molingana ndi chiŵerengero cha anthu ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

54 Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:54
7 Mawu Ofanana  

Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao.


Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,


Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani.


Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.


Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.


Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?


M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa