Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu),
Numeri 22:36 - Buku Lopatulika Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumudzi wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Balaki atamva kuti Balamu wafika, adatuluka kukamchingamira ku mzinda wina wokhala pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, umene umachita malire a dziko la Mowabu, kumapeto kwake kwenikweni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaki atamva kuti Balaamu akubwera, anapita kukakumana naye ku mzinda wa Mowabu umene unali mʼmalire a Arinoni, mʼmphepete mwa dziko lake. |
Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu),
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake.
Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.
Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.
Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.
Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumize kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu?
Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.
Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.
Ndipo muja tinalanda dziko m'manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni;
Pamenepo anayenda m'chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu.
Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samuele anafika. Ndipo Saulo anamchingamira kukamlonjera iye.