Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:20 - Buku Lopatulika

20 Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Iwo adzayankha kuti, ‘Ukutu Mowabu wagwa, amchititsa manyazi, mlireni mofuula. Mulengeze ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wasanduka bwinja.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika. Lirani mwachisoni ndipo fuwulani! Lengezani ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wawonongedwa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:20
10 Mawu Ofanana  

Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu.


Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.


kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;


Pamenepo anayenda m'chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa