Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Numeri 22:11 - Buku Lopatulika Taonani, anthu awa adatuluka mu Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, anthu awa adatuluka m'Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ‘Anthu amene achokera ku Ejipito, adzaza dziko lonse. Bwerani tsono, muŵatemberere m'malo mwanga, mwina mwake ndidzatha kumenyana nawo nkhondo ndi kuŵapirikitsa.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’ ” |
Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Mowabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti,
Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandichitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu.
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.
Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.
koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m'dzanja lake.
Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake.