Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 21:29 - Buku Lopatulika

Tsoka kwa iwe, Mowabu! Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu, anapereka ana ake aamuna opulumuka, ndi ana ake aakazi akhale ansinga, kwa Sihoni mfumu ya Aamori.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tsoka kwa iwe, Mowabu! Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu, anapereka ana ake amuna opulumuka, ndi ana ake akazi akhale ansinga, kwa Sihoni mfumu ya Aamori.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsoka kwa iwe Mowabu, mwatha inu anthu opembedza Kemosi. Ana ake aamuna waasandutsa othaŵathaŵa, ana ake aakazi waasandutsa akapolo, akapolo a Sihoni mfumu ya Aamori.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsoka kwa iwe Mowabu! Mwawonongedwa inu anthu a ku Kemosi! Ana ake aamuna wawasandutsa ngati anthu othawathawa ndipo ana ake aakazi ngati akapolo, akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori.

Onani mutuwo



Numeri 21:29
12 Mawu Ofanana  

Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.


Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, paphiri lili patsogolo pa Yerusalemu.


Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la chionongeko, imene Solomoni mfumu ya Israele adaimangira Asitaroti chonyansa cha Asidoni, ndi Kemosi chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu chonyansa cha ana a Amoni.


Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.


Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.


Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.


Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako aamuna atengedwa ndende, ndi ana ako aakazi atengedwa ndende.


Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Chimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simuchilandira cholowa chanu kodi? Momwemo aliyense Yehova Mulungu wathu waingitsa pamaso pathu, zakezo tilandira cholowa chathu.