Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:28 - Buku Lopatulika

28 Popeza moto unatuluka mu Hesiboni, chirangali cha moto m'mzinda wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Popeza moto unatuluka m'Hesiboni, chirangali cha moto m'mudzi wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Moto udabuka ku Hesiboni. Malaŵi a moto adatuluka mu mzinda wa Sihoni. Moto udaononga Ari mzinda wa ku Mowabu, udapserezeratu mapiri a kumtunda kwa Arinoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 “Moto unabuka ku Hesiboni, malawi a moto kuchokera mu mzinda wa Sihoni. Unanyeketsa Ari mzinda wa ku Mowabu, nzika za ku malo okwera a Arinoni.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:28
20 Mawu Ofanana  

Moto unapsereza anyamata ao; ndi anamwali ao sanalemekezeke.


Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.


Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.


Ndipo padzakhala kuti pamene Mowabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika kumalo ake oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.


koma ndidzatumiza moto pa linga la Tiro, ndipo udzanyeketsa nyumba zake zachifumu.


koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira.


koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu;


koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi.


koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu;


koma ndidzatumiza moto pa Mowabu, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Keriyoti; ndipo Mowabu adzafa ndi phokoso, ndi kufuula, ndi mau a lipenga;


koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za mu Yerusalemu.


ndi zigwa za miyendoyo zakutsikira kwao kwa Ari, ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu.


Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mzinda wa Sihoni umangike, nukhazikike.


Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.


Lero lomwe utumphe malire a Mowabu, ndiwo Ari.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.


Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero utuluke moto m'nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebanoni.


koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa