Numeri 21:29 - Buku Lopatulika29 Tsoka kwa iwe, Mowabu! Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu, anapereka ana ake aamuna opulumuka, ndi ana ake aakazi akhale ansinga, kwa Sihoni mfumu ya Aamori. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Tsoka kwa iwe, Mowabu! Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu, anapereka ana ake amuna opulumuka, ndi ana ake akazi akhale ansinga, kwa Sihoni mfumu ya Aamori. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Tsoka kwa iwe Mowabu, mwatha inu anthu opembedza Kemosi. Ana ake aamuna waasandutsa othaŵathaŵa, ana ake aakazi waasandutsa akapolo, akapolo a Sihoni mfumu ya Aamori. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Tsoka kwa iwe Mowabu! Mwawonongedwa inu anthu a ku Kemosi! Ana ake aamuna wawasandutsa ngati anthu othawathawa ndipo ana ake aakazi ngati akapolo, akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori. Onani mutuwo |