Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 48:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Motero Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi, mulungu wake, monga momwe Israele adachitira naye manyazi Betele, mulungu amene ankamukhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi, monga momwe Aisraeli anachitira manyazi ndi Beteli amene ankamukhutulira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:13
21 Mawu Ofanana  

Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.


Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, paphiri lili patsogolo pa Yerusalemu.


Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditse anthu ao m'dzanja lanu?


Ndipo padzakhala kuti pamene Mowabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika kumalo ake oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.


Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;


Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m'masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.


Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.


Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao.


Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.


Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako aamuna atengedwa ndende, ndi ana ako aakazi atengedwa ndende.


Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.


Chimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simuchilandira cholowa chanu kodi? Momwemo aliyense Yehova Mulungu wathu waingitsa pamaso pathu, zakezo tilandira cholowa chathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa