Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.
Numeri 21:18 - Buku Lopatulika chitsime adakumba mafumu, adachikonza omveka a anthu; atanena mlamuli, ndi ndodo zao. Ndipo atachoka kuchipululu anamuka ku Matana; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chitsime adakumba mafumu, adachikonza omveka a anthu; atanena mlamuli, ndi ndodo zao. Ndipo atachoka kuchipululu anamuka ku Matana; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chitsime chimene adakumba mafumu, chimene atsogoleri omveka a anthu adakumba, adakumba ndi ndodo zao zaufumu ndiponso ndi ndodo zao zoyendera.” Kuchokera kuchipululu, Aisraele adafika ku Matana, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero chitsime chomwe anakumba mafumu, chomwe anakumba anthu omveka, ndi ndodo zawo zaufumu ndi ndodo zawo zoyendera.” Kenaka anachoka ku chipululu ndi kupita ku Matana. |
Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.
Ndi pambali pao anakonza Atekowa; koma omveka ao sanapereke makosi ao kuntchito ya Mbuye wao.
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m'dziko limene ndiwapatsa likhale laolao.
Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?