Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma.
Numeri 20:9 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatenga ndodoyo kuichotsa pamaso pa Yehova, monga Iye anamuuza iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatenga ndodoyo kuichotsa pamaso pa Yehova, monga Iye anamuuza iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Mose adatenga ndodo imene inali pamaso pa Chauta, monga momwe Iyeyo adamlamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose anatenga ndodo pamaso pa Yehova monga momwe anamulamulira. |
Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma.
Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.