Numeri 2:27 - Buku Lopatulika Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Asere; ndi kalonga wa ana a Asere ndiye Pagiyele mwana wa Okarani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo a kumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Asere; ndi kalonga wa ana a Asere ndiye Pagiyele mwana wa Okarani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Asere, limene mtsogoleri wake ndi Pagiyele mwana wa Okarani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Fuko la Aseri lidzamanga pafupi ndi iwowo. Mtsogoleri wa Aaseri ndi Pagieli mwana wa Okirani. |
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Pagiyele mwana wa Okarani.