Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.
Numeri 2:17 - Buku Lopatulika Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pamenepo mpamene anyamule chihema chamsonkhano, chifukwa zithando za Alevi zimakhala pakati pa zithando zina. Monga momwe adamangira zithando zao, ndimo aziyendera, gulu lililonse pamalo pake motsatira mbendera yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake. |
Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.
Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.
Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.
Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe.
Pakuti ndingakhale ndili kwina m'thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.