Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Numeri 16:45 - Buku Lopatulika Kwerani kuchoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwerani kuchoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Choka pakati pa gulu la anthuli, kuti ndiŵaononge onse nthaŵi imodzi.” Aŵiriwo adadziponya pansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Chokani pakati pa gulu la anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.” Ndipo iwo anagwa pansi chafufumimba. |
Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kuchoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.
Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.
Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kunka ku khomo la chihema chokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.
Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.