Genesis 19:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene anakwata ana ake akazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Pamenepo Loti adapita kwa anyamata amene ankafuna kukwatira ana akewo naŵauza kuti, “Fulumirani, tiyeni tituluke kuno, chifukwa patsala pang'ono kuti Chauta aononge malo ano.” Koma iwowo ankangoyesa nthabwala chabe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula. Onani mutuwo |