ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;
Numeri 14:4 - Buku Lopatulika Ndipo anati wina ndi mnzake, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati wina ndi mnzake, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri kuti tibwerere ku Ejipito.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anawuzana wina ndi mnzake kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri ndipo tibwerere ku Igupto.” |
ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;
koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji mu Ejipito?
Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israele.
amene makolo athu sanafune kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,
Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.
Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, panjira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.