Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 14:25 - Buku Lopatulika

Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimumke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono popeza kuti Aamaleke ndi Akanani amakhala m'zigwa, maŵa mubwerere, muyambepo ulendo wopita ku chipululu, mudzere ku Nyanja Yofiira.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo popeza kuti Aamaleki ndi Akanaani akukhala ku chigwa, mawa mubwerere ndipo mupite ku chipululu podzera ku Nyanja Yofiira.”

Onani mutuwo



Numeri 14:25
7 Mawu Ofanana  

momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao.


Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.


Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,


Ndipo anati wina ndi mnzake, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Ejipito.


Koma inu, bwererani, mukani ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.


pakuti pakukwera iwo kuchokera ku Ejipito Israele anayenda m'chipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;