Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.
Numeri 13:31 - Buku Lopatulika Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitingathe kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitikhoza kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono anthu aja amene adaapita naye limodziŵa adati, “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, poti ngamphamvu kopambana ife.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.” |
Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.
Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israele kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?
Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.
Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.
Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, mizinda yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,
Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.
Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake.