Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.
Numeri 13:2 - Buku Lopatulika Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikupatsa Aisraele. Pa fuko lililonse utume munthu mmodzi, amene ali mtsogoleri m'fukolo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.” |
Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.
Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mafuko onse; yense mkulu wa nyumba ya kholo lake.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.
Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.
Ndipo Mose anawatumiza kuchokera ku chipululu cha Parani monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akulu a ana a Israele.
Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao.
Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu.
Ndipo pamene Yehova anakutumizani kuchokera ku Kadesi-Baranea, ndi kuti Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ake.
Ndipo tsono, mudzitengere amuna khumi ndi awiri mwa mafuko a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi.