Numeri 12:9 - Buku Lopatulika Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Chauta adaŵakwiyira, nachokapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anawakwiyira, nachoka. |
Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.
Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.
Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.
Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.