Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 11:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mose adaŵamva anthu aja akulira m'mabanja mwao monse, aliyense atakhala pakhomo pa hema lake. Chauta adaapsa mtima kwambiri, ndipo nayenso Mose adaaipidwa nazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mose anamva anthu a banja lililonse akufuwula, banja lililonse pa khomo la tenti yake. Yehova anakwiya kwambiri ndipo Mose anavutikanso mu mtima.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 11:10
19 Mawu Ofanana  

koma anadandaula m'mahema mwao, osamvera mau a Yehova.


Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?


Chifukwa chake Yehova anamva, nakwiya; ndipo anayatsa moto pa Yakobo, ndiponso mkwiyo unakwera pa Israele.


Pakumva ichi Mulungu, anakwiya, nanyozatu Israele;


Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.


Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.


Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munachitiranji choipa mtumiki wanu? Ndalekeranji kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse?


Ndipo pakugwa mame pachigono usiku, mana anagwapo.


Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.


Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye.


Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna, ndi makanda ao.


Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.


Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa