Numeri 12:4 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adauza Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti, “Atatu nonsenu mubwere ku chihema chamsonkhano.” Ndipo onse atatuwo adapitadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yomweyo Yehova anati kwa Mose, Aaroni ndi Miriamu, “Bwerani ku tenti ya msonkhano nonse atatu.” Ndipo atatuwo anapitadi kumeneko. |
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri.