pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira, ndipo anapha mwa onenepa ao, nagwetsa osankhika a Israele.
Numeri 11:34 - Buku Lopatulika Ndipo anatcha malowo dzina lake Kibroti-Hatava; popeza pamenepo anaika anthu osusuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatcha malowo dzina lake Kibroti-Hatava; popeza pamenepo anaika anthu osusuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Mandaankhuli, chifukwa choti kumeneko ndiko kumene adakwirira anthu ankhuli. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake malowo anawatcha Kibiroti Hatava chifukwa pamenepo anakwirirapo anthu osusuka aja. |
pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira, ndipo anapha mwa onenepa ao, nagwetsa osankhika a Israele.
Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.