Numeri 11:28 - Buku Lopatulika Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yoswa, mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose, mmodzi mwa anthu ake osankhidwa aja, adati, “Mbuyanga Mose, aletseni amenewo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha kuti, “Mbuye wanga Mose, aletseni!” |
Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'chigono.
Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.
Ndipo atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose,