Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.
Numeri 10:22 - Buku Lopatulika Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Elisama mwana wa Amihudi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Elisama mwana wa Amihudi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Otsata mbendera ya zithando za fuko la Efuremu adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Elisama mwana wa Amihudi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Magulu a msasa wa Aefereimu anatsatira potsatira mbendera yawo. Elisama mwana wa Amihudi ndiye anali mtsogoleri wawo. |
Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.
Wa ana a Yosefe: wa Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri.