Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
Numeri 10:17 - Buku Lopatulika Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anagwetsa Kachisi; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula Kachisi, anamuka naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu atagwetsa chihema cha Mulungu, ana a Geresoni ndi ana a Merari, oyenera kunyamula chihema cha Mulungu, adanyamuka ulendo wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka. |
Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
Ndipo akati amuke nacho chihemacho, Alevi amgwetse, ndipo akati achimange, Alevi achiimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.
Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.
Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.
Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,
podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.