Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira.
Numeri 1:52 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele amange mahema ao, yense ku chigono chake, ndi yense ku mbendera yake, monga mwa makamu ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele amange mahema ao, yense ku chigono chake, ndi yense ku mbendera yake, monga mwa makamu ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele azimanga mahema ao m'magulumagulu, aliyense pa chithando chake, ndipo onse azimanga pafupi ndi mbendera yao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake. |
Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira.
Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.
Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.