Numeri 1:42 - Buku Lopatulika A ana a Nafutali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 A ana a Nafutali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa zidzukulu za Nafutali adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali: Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. |
owerengedwa ao a fuko la Asere, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu.
owerengedwa ao a fuko la Nafutali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.